2 Samuel 19:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano ine zaka zanga zakwana 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa zinthu zokondwetsa ndi zosakondwetsa? Kodi ine mtumiki wanu ndingathe kuzindikira kukoma kwake kwa zakudya kapena zakumwa? Kodi ine ndingathebe kumamvera kuimba kwa amuna ndi kwa akazi? Chifukwa chiyani ine mtumiki wanu ndikakhale ngati katundu wolemera wosanjikiza pa inu, mbuyanga mfumu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lero ndiri nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira cimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oyimba? Cifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.