2 Samuel 19:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonde, ingondilolani ine mtumiki wanu ndibwerere kuti ndikafere kumudzi kwathu, pafupi ndi manda a bambo wanga ndi a mai wanga. Koma suyu mwana wanga Kimuhamu, akhale mtumiki wanu. Iyeyu ndiye aoloke pamodzi ndi inu mbuyanga mfumu. Ndipo mumchitire chilichonse chimene chikukomereni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga ku manda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Cimamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumcitire cimene cikukomerani.