2 Samuel 19:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idapitirira mpaka kukafika ku Giligala, ndipo Kimuhamu adapita nao. Anthu onse a ku Yuda ndiponso theka la anthu a ku Israele, onse adaperekeza mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Kimuhamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Cimamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israyeli.