2 Samuel 19:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Aisraele onse adafika kwa mfumu, nadzafunsa kuti, “Chifukwa chiyani abale athu Ayuda achita ngati kukubani, nabwera ndi inu amfumu pamodzi ndi banja lanu ndi anthu anu onse, kuwoloka Yordani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, Aisrayeli onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakucotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lace pa Yordano, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?