2 Samuel 19:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayuda adayankha Aisraelewo kuti, “Chifukwa chake nchakuti mfumuyi ndi mbale wathu weniweni. Inu chakukwiyitsani nchiyani pamenepa? Kodi mfumu taidyera chiyani? Nanga yatipatsa mphatso yanji?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israele. Chifukwa mfumu ili ya chibale chathu; tsono mulikukwiyiranji pa mlandu umenewu? Tinadya konse za mfumu kodi? Kapena kodi anatipatsa mtulo uliwonse?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israyeli. Cifukwa mfumu iri ya cibale cathu; tsono mulikukwiyiranji pa mrandu umenewu? tinadya konse za mfumu kodi? kapena kodi anatipatsa mtulo uli wonse?