2 Samuel 19:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yowabu adaloŵa m'nyumba ya mfumu nakafika kwa mfumu, nati, “Inu lero mwachititsa manyazi ankhondo anu amene apulumutsa moyo wanu, ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu anafika ku nyumba ya mfumu, nati, Lero mwacititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu amuna ndi akazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono;