2 Samuel 19:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
poti inu mumakonda anthu odana nanu, ndipo mumadana ndi anthu okukondani. Lero ndiye mwatiwonetsa poyera kuti akalonga ndi ankhondo anu mulibe nawo kanthu. Ha, ndikudziŵa kuti Abisalomu adakakhala moyo, tonsefe nkufa, inu mukadakondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika