2 Samuel 19:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nyamukani tsono mutuluke, mukaŵalimbitse mtima ankhondo anu moŵakondweretsa. Ndithu ndikulumbira pali Chauta kuti, ngati simupita, onse akuthaŵani usiku uno. Ndipo zimenezi zidzakuipirani kwambiri kupambana zoipa zonse zimene zidakugweranipo kale, kuyambira muli mwana mpaka tsopano lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono nyamukani, muturuke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kuturuka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo cimeneci cidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.