2 Samuel 19:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Itamva zimenezi mfumu idanyamuka, nikakhala pansi pafupi ndi chipata. Choncho anthu onse atamva kuti mfumu ili ku chipata, adabwera pamaso pa mfumuyo. Nthaŵi imeneyo nkuti Aisraele atathaŵa, aliyense kunka kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye. Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pacipata, Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu irikukhala pacipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisrayeli adathawa, munthu yense ku hema wace.