2 Samuel 19:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo onsewo ankangokangana okhaokha. Ankati, “Mfumu Davide adatipulumutsa kwa adani athu, ndipo adatilanditsa kwa Afilisti. Koma tsopano watuluka m'dziko muno, kuthaŵa Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israyeli analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.