2 Samuel 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isiboseti mwana wa Sauli anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israyeli, nacita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide.