2 Samuel 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Yoabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anaturuka nakomana nao pa thamanda la Gibeoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.