2 Samuel 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono aliyense adagwira mutu wa mnzake nabaya mnzakeyo m'nthitimu ndi lupanga. Choncho onse 24 adafera limodzi. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula kuti Helikati-Hazurimu, ndipo ali ku Gibiyoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono aliyense anagwira mutu wa mnzake namubaya mnzakeyo mʼnthiti ndi mpeni ndipo onse anagwera pansi limodzi. Kotero malo amenewo ku Gibiyoni amatchedwa Helikati Hazurimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzace, nagwaza ndi lupanga lace m'nthiti mwa mnzaceo Comweco anagwa limodzi; cifukwa cace malo aja anachedwa Dera la Mipeni la ku Gibeoni.