2 Samuel 2:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abineri anabwereza kunena kwa Asaheli, Pambuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yoabu?