2 Samuel 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwake, ndi khalilo linatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye anakana kupambuka; cifukwa cace Abineri anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwace, ndi khalilo linaturuka kumbuyo kwace. Ndipo anagwako, nafera pomwepo, Ndipo onse akufika kumalo kumene Asaheli anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo.