2 Samuel 2:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yowabu ndi Abisai adayamba kuthamangitsa Abinere. Ndipo pamene dzuŵa linkaloŵa, adakafika ku phiri la Ama limene lili cha kuno kwa Giya, pa njira yopita ku chipululu cha Gibiyoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, pa njira ya ku chipululu cha Gibiyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoabu ndi Abisai anampitikitsa Abineri; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku citunda ca Ama, cakuno ca Giya, pa njira ya ku cipululu ca Gibeoni.