2 Samuel 2:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abinere adafuulira Yowabu namufunsa kuti, “Kodi tipitirirebe kumenyana mpakampaka? Monga sukudziŵa kuti mathero ake adzakhala oŵaŵa? Kodi udzaŵaletsa liti anthu ako kutithamangitsa ife abale ao?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Abineri anaitana Yoabu nati, Kodi lupanga lidzaononga cionongere? sudziwa kodi kuti kutha kwace kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao?