2 Samuel 2:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu adabwerako kumene adaakathamangitsa Abinere kuja. Atasonkhanitsa anthu onse pamodzi, kudapezeka kuti padasoŵa ankhondo a Davide okwanira 19, pamodzi ndi Asahele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yowabu anabwerera kuchokera kothamangitsa Abineri ndipo anasonkhanitsa ankhondo ake onse. Kupatula Asaheli, panali ankhondo khumi ndi anayi a Davide amene anasowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu anabwerera pakutsata Abineri. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asaheli.