2 Samuel 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu a ku Yuda adafika, ndipo kumeneko adadzoza Davide kuti akhale mfumu yao. Davide atamva kuti ndi anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene adaika Saulo m'manda,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda. Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Jabezi Gileadi ndiwo amene anamuika Sauli.