2 Samuel 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna. Paja mbuyanu Saulo adamwalira, ndipo anthu a mtundu wa Yuda andidzoza ine kuti ndikhale mfumu yao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono manja anu alimbike, nimucite camuna; pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao.