2 Samuel 20:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Amasa sadaachenjera nalo lupanga limene linali m'dzanja lina la Yowabu. Pomwepo Yowabuyo adamubaya nalo lupangalo m'mimba kamodzi kokha, mpaka matumbo ake kukhuthuka, naafa pomwepo. Tsono Yowabu ndi Abisai mbale wake adalondola Sheba mwana wa Bikiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Amasa sanasamalira lupanga liri m'dzanja la Yoabu; comweco iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ace pansi, osamgwazanso; nafa iye, Ndipo Yoabu ndi Abisai mbale wace analondola Seba mwana wa Bikri.