2 Samuel 20:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina mwa ankhondo a Yowabu adakaimirira pambali pa mtembo wa Amasa, nati, “Aliyense wokhumba Yowabu ndi Davide, mlekeni atsate Yowabuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mnyamata wina wa Yoabu anaima pali iye, nati, Wobvomereza Yoabu, ndi iye amene ali wace wa Davide, atsate Yoabu.