2 Samuel 20:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu onse amene anali ndi Yowabu adabwera, nadzamzinga ndi zithando zankhondo Shebayo ku Abele wa ku Betemaki. Tsono adauundira mitumbira yankhondo mzindawo, nikagunda ku linga. Choncho ankagumula khoma kuti aligwetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza nammangira misasa m'Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza nammangira misasa m'Abeli wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda tioga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yoabu anakumba lingalo kuti aligwetse.