2 Samuel 20:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.” Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yoabu kodi? iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndirikumva.