2 Samuel 20:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Aisraele onse adaleka kumtsata Davide, nayamba kutsata Sheba, mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda adakhalabe nganganga pambuyo pa mfumu yao, kuyambira ku Yordani mpaka ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco anthu onse a Israyeli analeka kutsata Davide, natsata Seba mwana wa Bikri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordano kufikira ku Yerusalemu.