2 Samuel 20:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Cholinga si chimenechi. Koma munthu wina wa ku dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri, adaukira mfumu Davide. Mumpereke yekhayo, ndipo mzindawu ndiwuleka.” Mkazi uja adauza Yowabu kuti, “Tikuponyerani mutu wake pa khoma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.” Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mranduwo soli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efraimu, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri, anakweza dzanja lace pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzacoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yoabu, Onani tidzakuponyerani mutu wace kutumphitsa Gnga.