2 Samuel 20:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka pamudzipo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yace. Ndipo iwo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikri, nauponya kunja kwa Yoabu. Ndipo analiza Gpenga, nabalalika kucoka pamudzipo, munthu yense kumka ku hema wace. Ndipo Yoabu anabwerera kumka ku Yerusalemu kwa mfumu.