2 Samuel 20:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide atafika ku nyumba yake ku Yerusalemu, adatenga azikazi ake khumi amene adaaŵasiya kuti azisunga mudzi, naŵatsekera m'nyumba m'mene adaaikamo mlonda woŵalonda. Ankaŵapatsa chakudya, koma Davide sankaloŵa m'nyumbamo kwa akaziwo. Adaŵatsekera m'nyumba choncho mpaka tsiku la kufa kwao, ndipo ankakhala ngati akazi amasiye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide anafika kunyumba kwace ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa cakudya, koma sanalowana nao. Comweco iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye.