2 Samuel 20:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene adafika ku mwala waukulu umene uli ku Gibiyoni, Amasa adabwera kudzakumana nawo. Tsono Yowabu adaavala malaya ankhondo, ndipo pamwamba pa malayawo m'chiwuno mwake, panali lamba womangirirapo lupanga lam'chimake. Pamene ankayenda, lidasololoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika iwo pa mwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika iwo pa mwala waukuru uli ku Gibeoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yoabu atabvala mwinjiro wace, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'cimace m'cuuno mwace; ndipo m'kuyenda kwace lidasololoka.