2 Samuel 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yowabu adafunsa Amasa kuti, “Kodi nkwabwino mbale wanga?” Pamenepo Yowabuyo adamgwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja kuti amumpsompsone.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yoabu anagwira ndebvu za Amasa ndi dzanja lace lamanja kuti ampsompsone.