2 Samuel 21:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ya ufumu wa Davide kunali njala ya zaka zitatu motsatanatsatana. Ndiye Davide adapempha nzeru kwa Chauta, ndipo Chauta adamuuza kuti, “Saulo ndi banja lake adakali nawobe mlandu uja wopha Agibiyoniwu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'masiku a Davide munali odala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndico cifukwa ca Sauli ndi nyumba yace yamwazi, popeza iye anawapha Agibeoni.