2 Samuel 21:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rizipa, mwana wamkazi wa Aya, adatenga chiguduli nadziyalira pathanthwe pamene panali mitembo ya anthuwo, kuyambira pa chiyambi cha kholola mpaka mvula idayambanso kugwa. Mkaziyo sadalole kuti pa mitemboyo pafike mbalame masana kapena zilombo zakuthengo usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo za kuthengo usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga ciguduli, nadziyalira ici pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ocokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zirombo za kuthengo usiku.