2 Samuel 21:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adapita kukatenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wa Saulo. Adaŵachotsa m'manja mwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, amene adaaba mafupawo ku bwalo la ku Beteseani, kumene Afilisti adaaŵanyonga, tsiku limene Afilistiwo adapha Saulo ku Gilibowa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;