2 Samuel 21:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide adatenga mafupa a Saulo ndi a Yonatani mwana wake naŵachotsa kumeneko. Kenaka adasonkhanitsanso mafupa a anthu aja amene adaŵanyongera paphiri paja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nacotsa kumeneko mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapacikidwa.