2 Samuel 21:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adaika mafupa a Saulowo pamodzi ndi mafupa a Yonatani mwana wake, m'dziko la Benjamini ku Zela, m'manda a Kisi bambo wake wa Saulo, potsata zonse zimene mfumu idaalamula. Pambuyo pake Mulungu adamvera mapemphero opempherera dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naika mafupa a Sauli ndi Jonatani mwana wace ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wace; nacita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pace Mulungu anapembedzeka za dzikolo.