2 Samuel 21:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, amene mkondo wake unkalemera makilogramu atatu ndi theka, ndiponso amene anali ndi lupanga latsopano m'lamba, adaganiza zoti aphe Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Isibenobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wace kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anabvala lupanga latsopano, nati aphe Davide.