2 Samuel 21:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka nkhondo inanso idabuka ndi Afilisti omwewo ku Gobu. Tsono Elihanani, mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu, adapha Lahimi, mbale wa Goliyati wa ku Gati uja, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elhanani mwana wa Jare-oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliate Mgiti, amene mtengo wa mkondo wace unanga mtanda wa woombera nsaru.