2 Samuel 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumuyo idaitana Agibiyoni. Agibiyoniwo sanali Aisraele, koma Aamori otsalira. Ngakhale Aisraele anali atalumbira kuti sadzaŵapha Agibiyoniwo, komabe Saulo adafuna kuŵaonongeratu chifukwa cha chikondi chake pa Israele ndi pa Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda).
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inaitana Agibeoni, ninena nao (koma Agibeoni sanali a ana a Israyeli, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israyeli anawalumbirira kwa iwo, koma Sauli anafuna kuwapha mwa cangu cace ca kwa ana a Israyeli ndi a Yuda).