2 Samuel 21:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudabukanso nkhondo ina ku Gati, kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene anali nazo zala zisanu ndi cimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi cimodzi kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.