2 Samuel 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Davide adafunsa Agibiyoni aja kuti, “Kodi ndikuchitireni chiyani? Ndingapepese bwanji kuti mutipemphere kwa Chauta kuti atidalitse?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Davide ananena ndi Agibeoni, Ndidzakucitirani ciani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi ciani kuti mukadalitse colowa ca Yehova?