2 Samuel 21:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Agibiyoniwo adauza Davide kuti, “Mlandu umene ulipo pakati pa ife ndi Saulo kapena banja lake, si woti nkulipira ndi golide kapena siliva, ndiponso sikuti kapena ife tikufuna kulipira pakupha wina aliyense m'dziko la Israele ai.” Apo Davide adafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndikuchitireni chiyani?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa m'Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.” Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Agibeoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golidi wa Sauli kapena nyumba yace; ndiponso sitifuna kupha munthu ali yense wa m'Israyeli. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakucitirani.