2 Samuel 21:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwa zidzukulu zake mutipatse anthu asanu ndi aŵiri, kuti ife tikaŵanyonge pamaso pa Chauta ku Gibiyoni, ku mzinda wa Saulo munthu wosankhidwa wa Chauta.” Apo mfumuyo idayankha kuti, “Chabwino, ndidzaŵapereka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutipatse ana ake amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova m'Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mutipatse ana ace amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapacika kwa Yehova m'Gibeya wa Sauli, wosankhika wa Yehova, Mfumu niti, Ndidzawapereka.