2 Samuel 21:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumuyo idatenga Arimoni ndi Mefiboseti winanso, ana a Rizipa, mwana wamkazi wa Aya amene adambalira Saulo. Idatenganso ana aamuna asanu amene Merabi, mwana wamkazi wa Saulo, adambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Sauli, ndiwo Arimoni ndi, Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, amene iye anambalira Adriyeli mwana wa Barizilai Mmeholati;