2 Samuel 22:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mudandipulumutsa kwa anthu anga ondiwukira. Mudandisunga kuti ndikhale wolamulira mitundu yonse. Choncho anthu osaŵadziŵa adayamba kunditumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwa adzanditumikira ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.