2 Samuel 22:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga. Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene anditurutsa kwa adani anga; Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.