2 Samuel 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga, ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali m'Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; Ndipo Iye anamva mau anga ali m'kacisi wace, Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.