2 Samuel 22:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima chifukwa Chauta adaakalipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika Nagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.