2 Samuel 23:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa mau otsiriza a Davide: Nayi nyimbo ya Davide, mwana wa Yese, mau a munthu amene Mulungu adamkweza pamwamba, amene Mulungu wa Yakobe adamdzoza kuti akhale mfumu, munthu wokonda kuimba nyimbo zokoma za Israele:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa, Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:— Atero Davide mwana wa Jese, Atero munthu wokwezedwa, Ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, Ndi mwini masalmo wokoma wa Israyeli: