2 Samuel 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iyeyo adatsalira, nakantha Afilisti mpaka dzanja lake kuchita kutopa, komabe osataya lupanga. Tsiku limenelo Chauta adampambanitsa. Aisraelewo adabwerera pambuyo pake kudzangofunkha za ophedwawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lace linalema, ndi dzanja lace lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwace kukafunkha kokha.