2 Samuel 23:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthu atatu amphamvu aja adapita, nabzola zithando za Afilisti, nkutunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo, nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo adangoŵathira pansi, kuŵapereka kwa Chauta,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipongwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'citsime ca ku Betelehemu, ca pa cipataco, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafuna kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.